"TIYAMBE NDI KUKHALA NDI TIMU YABWINO KENAKO ZOTSATIRA" - MPONDA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Flames wogwirizira, Peter Mponda, wati anthu asayembekezere za zotsatira zabwino kutimuyi posachedwa pomwe khumbo lawo ndi lomanga kaye timu ya mphamvu yomwe ikadzagwirana idzachite bwino.
Iye amayankhula pomwe timu ya dziko lino yayamba zokonzekera mu mzinda wa Lilongwe patsogolo pa masewero awo ndi Burundi komanso Burkina Faso mwezi womwe uno.
Iye wati zokonzekera zawo zayamba bwino ngakhale kuti anayamba ndi osewera ocheperako poti a Mighty Mukuru Wanderers anachita kuchokera ku Blantyre poti anasewera lamulungu.
Iye wati khumbo lawo ndi kumanga timu yomwe ikhale kuchita bwino mu kanthawi kakudzaka osati lero ndi lero.
"Chimene tiyang'ane kwambiri ndi kuti timange timu yabwino yomwe ikagwirana idzatibweretsera zotsatira zabwino, timu yoti tiyipatse mbali komwe ikulowera chifukwa mmbuyomu simachita bwino koma tsopano iyambe kuchita bwino nde timange timu yabwino kenako zotsatira p
pambuyo." Anatero Mponda.
Iye anatinso anthu amadandaula kuti aphunzitsi onse omwe amabwera kutimuyi amati akufuna akonze timu koma Iwo ayike ndondomeko zoyenera kuti zithekedi ndikukhala nditimu yopambana kwambiri.
Timuyi yomwe ikutsogozedwa ndi mphunzitsi waku Zimbabwe, Kalisto Pasuwa, yachititsa kuti osewera omwe anasowa kutimuyi, Richard Mbulu, Gabadinho Mhango ndi Charles Petro abwererenso kutimuyi.
Ngakhale timuyi ikusewera mmasewero opitira ku African Cup of Nations, matimu a Senegal ndi Burkina Faso ndiomwe anapita kale kumpikisanowu kuchokera mu gulu pomwe muli Malawi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores