GONDWE WADZUDZULA KHALIDWE LA GABA
Osewera wakale wa timu ya Flames, Chancy Gondwe, waonetsa kudandaula ndi khalidwe la katswiri wa mdziko lino, Gabadinho Mhango, kutsatira kuchita zinthu zosayenera ngati kukonda kabanga komanso amayi.
Iye amayankhula ndi tsamba lamdziko la South Africa la Kick off pomwe katswiriyu anapezeka pa kanema yemwe anazungulira mmasamba amchezo atachita ngozi pomwe mu galimotoyo munali atsikana komanso zikumveka kuti inali mphamvu ya mowa.
Gondwe wati khalidwe lomwe akupanga katswiriyu ndi losayenera poti osewerayu amakondedwa kwambiri mdziko lake koma akuoneka kuti khalidwe lake ndi lonunkha ndithu.
"Ndi zokhumudwitsa kuti zimenezi zachitikira mmodzi mwa ife. Gaba ku Malawi ndi mulungu koma khalidwe lake silikugwirizana ndi osewera wapamwamba, za mowa ndi azimayi zimangoyipitsa mbiri koma zilibe phindu lililonse lomwe munthu angapezeko." Anatero Gondwe.
Iye wati nkhani imeneyi ikanachitikira munthu yemwe si otchuka ngati iyeyu sikanapita patali koma poti
ndi iyeyu yapita patali zomwe ndi zosafunikira kumapetopeto kwa kusewera mpira kwake.
Gondwe anakambakonso kuti mphunzitsi ndi osewera wakale wa Flames, Ernest Ntawali, amakhala akumuyankhula katswiriyu zokhudza khalidwe lake koma akuoneka kuti khalidwe lake ndi lakelake basi.
Ndipo mkhalapakati wa osewerayu, Mike Makaab poyankhulapo za nkhaniyi anati sathilirapo mlomo mpaka apolisi omwe akufufuza amalize kafukufuku wawo komanso timu yake.
Mu ligi ya 2024/25 Betway Premiership ku South Africa, Mhango wakwanitsa kungogoletsa chigoli chimodzi pa masewero atatu pomwe masewero ndi Amazulu sanasewere nawo.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores