"OSEWERA ANATOPA CHIFUKWA BUS INAFA" - YASIN
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Rodgers Yasin, wati zinali zovuta kuti timu yawo ipeze chipambano poti afika mochedwa ku Karonga kamba koti galimoto yawo yoyendera inaonongeka ku Lilongwe.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 4-0 ndi Chitipa United ndipo wati kuchezera mausiku awiri akuyenda ndi kusapuma zapangitsa iwo kuti asachite bwino osati Kadi yofiira yomwe osewera wawo anapatsidwa.
"Chomwe ndinganene ndi choti zinali zovuta kupambana chifukwa osewera atopa. Galimoto inationongekera pa Lumbadzi tikubwera Juno nde tinathapo tsiku tili pomwepo tinachita kubwereka ina nde tafika mmawa wa lero zinali zovuta." Anatero Yasin.
Iye anati timuyi yapezetsa zigoli zophweka kwambiri ndipo kadi yofiyira yomwe Gabinho Daudi anapatsidwa sangadandaule chifukwa osewera amayenera azikhala ndi khalidwe.
Timuyi tsopano ili pa nambala 15 pomwe ili ndi mapointsi 12 pa masewero 17 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores