MAPHUNZIRO A VAR AKUYAMBA LERO
Bungwe la Football Association of Malawi lalengeza kuti maphunziro a oyimbira a masiku asanu a mayiko omwe ali pansi pa bungwe la FIFA akuyambika mtsiku la lero ku Mpira Village ku Blantyre.
Maphunzirowa ayitanitsa oyimbira 35 kuchokera mmadera osiyanasiyana mdziko muno ndipo pamwamba pa maphunzirowa, Iwo aphunziranso kagwiritsidwe ka makina atsopano a kanema omwe amathandizira kuyimbira (Video Assistant Referee)
Izi zikudza pomwe mtsogoleri wa bungweli, Fleetwood Haiya, analengeza posachedwa kuti makinawa ayamba kugwira ntchito mdziko muno posachedwapa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores