"TIDIKIRA TIKAMBIRANE KALE KOMA SINATIPEZE" - GONDWE
Mmodzi mwa akuluakulu atimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Chancy Gondwe, wati timu yawo siyinalandire kalata yomwe mphunzitsi watimuyi, Nsanzurwimo Ramadan wapereka kuti wasiya ntchito koma ikafika ayikhalira pansi ndikukambirana ngati akuluakulu.
Iye wayankhula izi kutsatira malipoti osonyeza kuti Ramadan watsanzika kutimuyi ndipo Gondwe wati padakali panopa sangayankhulepo zambiri poti kalatayi sinafike.
"Ndayiona pa Nation Online zoti wapita koma kalatayo sinatipeze koma ngati itatipeze tiyikhalira pansi ngati board komanso a pulezidenti athu ndipo tiona kuti chitsogolo ndi chotani koma padakali panopa sindingayankhule za mmutu mwanga, tikumane kaye." Anatero Gondwe.
Iye wati ayiunikira bwinobwino kalatayo kuti awone zofooka ndi zina zomwe mphunzitsiyu walembamo kenako chiganizo chotsatira adzachinena kwa anthu.
Mphunzitsiyu anafika mdziko muno pa 1 March 2024 kudzaphunzitsa timuyi ndipo watsogolera mmasewero asanu ndi atatu (
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores