"TIKUMAPEMPHERA KWAMBIRI KUTIMU YATHU" - NGINDE
Mphunzitsi watimu ya Creck Sporting Club, Macdonald Mtetemera, wati makhalidwe a osewera kutimuyi akhala abwino poti akumawalimbikitsa kupemphera.
Nginde amayankhula atapambana 3-1 pamwamba pa Mighty Waka Waka Tigers kuti afike pamtunda penipeni pa ligi. Iye wati timu yake ikutsogoza mapemphero malingana ndi mbiri yatimuyi.
"Osewera ngati Hadji Wali tikumangopempherera kuti mwina khalidwe likhaleko labwino ndipo muwaona akuchita bwino. Timu yathuyi ndi ya ana kwambiri nde zina tikhale tikuphunzirabe." Anatero Mtetemera.
Timuyi yangolowa kumene ndipo ilibe mbiri iliyonse yakusewera mu ligi yaikuluyi ndipo ili pamwamba ndi mapointsi atatu mu sabata yoyamba.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores