"NDINE WOKONDWA POTI TAFIKA NDIME INA" - KUMILAMBE
Mphunzitsi watimu yomwe imasewera masewero apagombe ya dziko lino, Willy Kumilambe, wati ndi wokondwa poti timu yake yafika mu ndime yamatimu anayi ndipo ayesetsa kuchita bwino kuti amalize mwapamwamba.
Iye amayankhula atatha masewero omwe anagonjetsa Seychelles 7-2 masana a lachitatu ndipo wati amadziwa kuti apambana.
"Ndine okondwa kwambiri kuti tafika mu ndime ina chifukwa masewero alero tinali ndi phuma poti kugonja Kwa dzulo tinazipatsa ntchito yaikulu komabe timadziwa kuti tiwina." Anatero Kumilambe.
Iye wayamikira osewera omwe anasewera masewero awo koyamba kuti ayithandiza timuyi ndipo tsogolo lilipo lamphamvu.
Malawi ikumana ndi Morocco lachisanu mu ndime ya matimu anayi pomwe Saudi Arabia ikumana ndi Mozambique mu maseweronso ena.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores