"TABWERA KUNO KUDZAPANGA ZENIZENI" - KUMILAMBE
Mphunzitsi watimu ya dziko lino yapagombe, Willy Kumilambe, wati kupambana kwa timuyi ndi eni khomo a South Africa ndi chidziwitso kuti apita kuti akagwire ntchito.
Iye amayankhula atatha masewero omwe anachokera kumbuyo ndikugonjetsa South Africa 4-2 pa bwalo la South Beach Soccer lamulungu ndipo wati sanali masewero ophweka.
"Anali masewero ovuta kutengera kuti mukamasewera ndi eni khomo pamakhala zambiri zoti zili kumbali yawo. Sapoti komanso bwalo akulidziwa nde gawo loyamba ndi lachiwiri tinavutika koma lachitatu nde tinabwera bwinobwino." Anatero Kumilambe.
Iye wati masewero omwe akusewera ndi Saudi Arabia lolemba nde ali ovuta kwambiri poti ku mayiko a Aluya ndi kuchimake kwa akatswiri a mpikisanowu komabe wati alimbikira.
Aka ndi kachiwiri timuyi kutenga nawo mbali mu mpikisano wa COSAFA pomwe nthawi yoyamba anathera pa nambala yachitatu ku Mozambique.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores