"CHILICHONSE CHITHA KUCHITIKA" - CHATAMA
Mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets Reserve, Enos Chatama, wati akudziwa kuti masewero ndi FOMO akhala ndi mwayi wochepa komabe wati chilichonse chimachitika mu masewero a mpira wamiyendo.
Iye amayankhula patsogolo pa kukumana kwa matimuwa pa bwalo la Kamuzu lachitatu ndipo wati anyamata ake akonzeka kugwira ntchito.
"Akhala masewero ovuta ndipo FOMO ili ndi mwayi waukulu woti ipitilira komabe pa bwalo takonzekera, anyamata tawauza kuti chilichonse mu mpira chikhonza kuchitika nde takonzeka kwambiri." Anatero Chatama.
Timuyi ikupita mmasewerowa ikutsalira 2-0 kutsatira kugonja mmasewero oyamba ku Mulanje. Opambana lero akumane ndi Ntopwa mu ndime yotsiriza.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores