"SIKUTI NDINE WABWINO KOMA NDILI KU TIMU YABWINO" - PHIRI
Wosewera watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Precious Phiri, wati kusewera bwino mu chaka cha 2023 kutimuyi sikuti iyeyo ali ndi luso kwambiri koma kuti ali kutimu yabwino.
Iye amayankhula pomwe amaonjezera mgwirizano wake ndi zaka zitatu kutimuyi ndipo kuti wasewera mmalo osiyanasiyana kutimuyi, iye wati amangotsatira zimene amauzidwa ndi aphunzitsi.
"Ndinalidi ndi chaka chabwino ndipo ndimathokoza aphunzitsi athu poti amatiuza zoti tichite, kusewera malo osiyanasiyana sikuti ndine waluso kwambiri koma kuchita zomwe ndauzidwa komanso ndili ku malo abwino omwe timamvako bwino." Anatero Phiri.
Katswiriyu anapambana mphoto zitatu za osewera wosewera bwino pamwezi kutimuyi chaka chatha ndipo anapita ku Bullets mu 2018 kuchokera ku Mighty Tigers.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores