THOM WAYAMBA BWINO KU TP MAZEMBE CHAKA CHINO
Katswiri womwetsa zigoli ku Scorchers, Sabina Thom, wayamba bwino mu ligi yaku DRC ya chaka chino ndi TP Mazembe pomwe lachitatu anagoletsa zigoli ziwiri ndikuthandizira chimodzi pomwe Mazembe yapha Bikira M.H. 6-0 mu ligi ya mdzikomo.
Awa anali masewero oyamba a ligiyi mu chaka cha 2024 ndipo Thom anachita monga mwa ntchito yake ndipo masewero ena alikonso lamulungu.
Osewera omwetsa zigoli amdziko muno monga Temwa, Tabitha Chawinga, Vitumbiko Mercy Mkandawire, Mary Chavinda komanso Thom akuchita bwino kwambiri pomwe akumwetsa zigoli kwambiri mmayiko momwe iwo ali.
Thom anagoletsa chigoli chopambanira chikho cha COSAFA Women's Championship pomwe Malawi inagweba Zambia 2-1.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores