MIPANDO 145 INAPHWANYIDWANSO PA BINGU
Bwalo la Bingu laulula kuti mipando yokwana 145 ndi imene inaonongedwa pa masewero a ndime yotsiriza ya chikho cha Castel Challenge pomwe matimu a FCB Nyasa Big Bullets ndi Silver Strikers ankakumana pa 31 December 2023.
Izi zaululika kutsatiranso kanema yemwe anazungulira pa tsamba la mchezo oonetsa masapota a Silver Strikers akuzula mipando ndi kumagendera anzawo a Bullets.
Zateremu ndekuti mipando yokwana 395 ndi imene yaonongedwa mu 2023 kutsatira kuti masapota a Wanderers anaphwanyanso mipando 240 ndipo anauzidwa kuti alipire K22.5 million.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores