MATIMU AYAMBA KUSAINA OSEWERA
Matimu osiyanasiyana ayamba ndi mphamvu posaina osewera kuti alimbitse matimu awo pomwe matimu a FCB Nyasa Big Bullets komanso Silver Strikers awonjezera kale anyamata lachitatu sabata ino.
Bullets yalengeza kuti yapereka K10 million komanso anyamata atatu omwe adziwike masiku akudzawa kuti atenge osewera wapakati wa Civo, Lloyd Aaron, yemwe atumikire mapale chaka chino.
Ndipo FCB Nyasa Big Bullets inamaliza kumvana ndi katswiri wa Blue Eagles, Christopher Gototo, koma Silver Strikers yapereka K5.5 million kuti itenge katswiriyu yemwe wasaina mgwirizano wa zaka zitatu.
Ena mwa osewera omwe akutchulidwa kwambiri kuti akufunidwa ndi Clement Nyondo komanso Charles Chipala onse a Dedza Dynamos, Innocent Nyasulu wa Tigers, Chris Lwemba wa Chitipa United komanso Robert Saizi wa Bangwe All Stars.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores