MABEDI WASAINA TSOPANO MGWIRIZANO WA ZAKA ZIWIRI
Mphunzitsi watimu ya dziko lino, Patrick Mabedi, tsopano wasaina mgwirizano wa zaka ziwiri ndi bungwe la Football Association of Malawi kutsatirano kumvana kwa mbali ziwirizi.
Mphunzitsiyu analengezedwa mu October kuti wapatsidwa mgwirizanowu koma anali asanasaine chifukwa panali zina zomwe samamvana mu mgwirizanowu.
Iye wati ndi wokondwa posaina mgwirizanowu tsopano patatenga nthawi ndipo tsopano akufuna amalizitse zimene anaziyamba kutimuyi mu miyezi imene wakhalako.
Mgwirizanowu wayambira pa 1 December 2023 ndipo ukuyembekezeka kudzatha pa 1 December 2025.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores