"NDI ANA NDE AKUFUNA KUZIPANGIRA MAYINA" - KAMWENDO
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Joseph Kamwendo, wayamikira anyamata ake kamba kochita bwino ndikufika mu ndime ya matimu anayi a Castel Challenge Cup ndipo wati akunjoya ndi mmene anyamatawa akuchitira.
Iye wati ndi zovuta kuti timu yoti yalowa kumene mu ligi yaikulu kumachita bwino ngati mmene ikuchitira pakadali pano ndipo wati ichi ndi chifukwa choti osewera atimuyi akulimbikira.
"Tikunjoya ndi mmene tikuchitira panopa ndi anyamata oti ali ndi chidwi kwambiri, akumalimbikira kwambiri chifukwa enawa abwera kumene mu ligi nde akufuna kuzipangira mayina ndi chifukwa tikumangowalimbitsa mtima popita mu bwalo la zamasewero." Anatero Kamwendo.
Timu ya Bangwe yakhala yoyamba kufika mu ndime anayi a Castel Challenge Cup itagonjetsa Chitipa United 3-4 pa mapenate ndipo kumbali ya ligi, iyo inathera pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) italolera mapointsi 42 pa masewero 30.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores