"TIKONZA TIMU YOOPSA KWAMBIRI CHAKA CHA MAWA" - MAKAWA
Mphunzitsi watimu ya Civo United, Abbas Makawa, wati akuyembekeza kuyankhulana ndi mabwana ake kuti akonze zinthu zingapo kutimuyi ndikuti apange timu yoopsa kwambiri mu chaka cha 2024.
Iye amayankhula izi atagonja 3-0 ndi FCB Nyasa Big Bullets pa bwalo la Kamuzu kuti atuluke mu chikho cha Castel ndipo anati zomwe anyamata anauzidwa sanapange koma akonza mu chaka cha mawa.
"Tinayesera kuwayankhula nthawi yopumulira koma poti ife sitimamenya sanamvere komabe kwatha kwa chaka chino tiyankhulana ndi mabwana kuti tikonze mavuto athu ndikuti tipange timu yoopsa kwambiri." Anatero Makawa.
Timu ya Civo inamaliza pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) mu ligi ya TNM itatolera mapointsi 37 pa masewero 30 omwe anasewera ndipo mu Airtel Top 8 ya chaka cha mawa adzakumananso ndi FCB Nyasa Big Bullets.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores