WANDERERS YAOPSEZA KUTENGA CHILETSO KU MAKHOTI A DZIKO
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yalembera bungwe la Football Association of Malawi kuyimitsa masewero aliwonse a Airtel Top 8 kufikira mlandu wawo utamveka ndipo kupanda kutero akasuma ku makhoti akunja kwa mpira.
Mu kalata yomwe wasaina ndi Council David Kanyenda yopita ku FAM kudzeranso kwa Airtel yati bungweli lisapitilire ndi masewero ena aliwonse a chikhochi kufikira mlandu wawo utaunikidwa ndi komiti yamilandu ya bungweli.
Iwo atinso FAM ichotse ndi kufufuta zomwe yakhala ikulemba mmasamba a mchezo zomwe ndi zabodza zoti iyo yagonja 2-0 ndipo masewero ena aliko kumapeto a sabatayi.
Iwo ati ngati zivute ndekuti akatenga chiletso ku khothi yosakhala yampira pofuna kuthandizira kuti chilungamo chiyende bwinobwino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores