"MATIMU AZIDZALANDIRA K20 MILLION CHAKA CHA MAWA" - HAIYA
Mtsogoleri wa bungwe la Super League of Malawi, Fleetwood Haiya, wati bungwe lawo likuthokoza Mulungu kamba koti zinthu zimene ankazilingalira kuti zichitika zatheka pomwe ena ankakaikira.
Iye amayankhula pa tsiku lotsiriza la ligiyi pomwe matimu a FCB Nyasa Big Bullets ndi Silver Strikers amakumana pa bwalo la Kamuzu ndipo wati zinthu zambiri zayenda pomwe zina zibweranso chaka cha mawa.
"Choyamba tithokoze Mulungu kuti chilichonse chayenda bwino mpaka pano tafika kumapeto kwa ligiyi. Mmene timaabweretsa Revive Rebrand and Reform ena amakaikira koma zatheka ndipo mpikisano unalipo chaka chino, zaka za mmbuyo chikho chimatengedwa kutatsala masewero ena komanso mpaka pano wotuluka sakudziwika ati masamu avuta." Anatero Haiya.
Iye anati zosewera kamodzi pa sabata komanso zopangiratu masewero zathandizira kukometsa masewero ndipo wati chaka cha mawa akonza mavuto omwe anakumana nawo.
"Ndalama yoyambira kumatimu inali K10 Milli
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores