"KUPULUMUKA KWAKE KOMA KOVUTA" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Pritchard Mwansa, wati phuma lomwe anali nalo tsopano latha kamba koti apulumuka mu ligi koma wati ntchito yake sinali yophweka.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa Blue Eagles 2-1 koyenda kuti atsalebe mu ligi ndipo wati ntchito ilipo chaka cha mawa kuti akonze timu yabwino.
"Phuma linali ndi ine koma apa latha kwatsala ndi koti chaka cha mawa tipange timu yabwino chifukwa MAFCO ndi timu yabwino ili ndi zoyenereza zonse zabwino nde sitikuyenera kumakhala malo ngati omwe tinaliwa. Mmasewero a lero sizinali zophweka poti Blue Eagles ndi timunso yabwino koma anyamata anamvera kwambiri lero." Anatero Mwansa.
Timu ya MAFCO yamaliza ligi ndi mapointsi 37 pa masewero 30 omwe yasewera ndipo ili pa nambala 10 mu ligiyi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores