"SIKUTI LINALI PHWANDO NAYO RED LIONS IMASEWERA" - CHINGOKA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Victor Chingoka, wati kupambana 7-0 ndi timu ya Red Lions sinali phwando kapena kupatsidwa koma wati ndi okondwa poti timuyi yatsala mu ligi.
Iye amayankhula atatha masewerowa omwe Gastin Simkonda anamwetsa zigoli zinayi, Raphael Phiri ziwiri ndi George Nyirenda chimodzi ndipo wati timu yake inasewera bwino kwambiri.
"Anali masewero abwino kwambiri lero anyamata anapita kutsogolo kwambiri nde zatithandiza kuti tipeze zigoli ndipo kumapetoku anyamata akulimbikira kwambiri nde ndine wokondwa kuti tatsalabe mu ligi. Sikuti linali phwando ayi chifukwa Red Lions nayonso imasewera bwino koma ikafika kutsogolo imaphonya kwambiri." Anatero Chingoka.
Timu ya Moyale yatsala mu ligi kamba koti inatenga mapointsi ambiri pa Blue Eagles yomwe anafanana nayo kalikonse ndipo yathera pa nambala 13 ndi mapointsi 35.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores