"SINDINAGANIZIREKO ZOTI TITULUKA" - CHIRAMBO
Mphunzitsi watimu ya Ekwendeni Hammers, Elias Chirambo, wati ndi wokondwa kamba koti timu yake yatsala mu ligi ya TNM Supa ligi ya chaka chino ndipo wati sanaganizireko zoti atuluka mu ligi.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonjetsa Dedza Dynamos 2-1 kuti apulumuke mu ligi ndipo wati anyamata ake analimbikira kwambiri mmasewerowa.
"Anali masewero abwino kwambiri ndipo tithokoze Mulungu kuti tapambana ndipo tili pa mapointsi 36, sindinaganizireko zotuluka mmutu mwangamu kungoti kumpoto tili ndi matimu abwino kwambiri koma kuti thandizo ndi lomwe limasowa kwambiri." Anatero CHIRAMBO.
Timu ya Ekwendeni Hammers inali imodzi mwa matimu omwe anali pa ngozi yotuluka koma chipambanochi chawafikira pa mapointsi 36 pa masewero 30 pa nambala 12.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores