"SINDINGAYANKHULEPO ZAMBIRI KUTI NDICHOKA" - NYONDO
Wosewera mbambande womwetsa zigoli kutimu ya Dedza Dynamos, Clement Nyondo, wati ndi wokondwa kamba kopambana mphoto ya wosewera womwetsa zigoli zambiri mu ligi ndipo wati alimbikirabe kuti chaka cha mawa adzachitenso bwino.
Iye amayankhula atatha masewero omwe timu yake yagonja 2-1 ndipo anagoletsa chigoli pa penate kuti zikwane 16 ndi kutenga mphotoyi. Iye wathokoza osewera anzake pomuthandiza kuti atenge mphotoyi.
"Ndine wokondwa kwambiri kuti ndapambana mphotoyi, sizinali zophweka koma ndinalimbikira kwambiri. Ndilimbikirabe kuti chaka cha mawa ndizachite bwino ndipo ndithokoze anzanga pondithandiza kuti ndapambane. Zoti ndichoka sindingayankhule zambiri poti sindikudziwa za mtsogolo." Anatero Nyondo.
Nyondo wamaliza ndi zigoli 16, ziwiri pamwamba pa katswiri wa FCB Nyasa Big Bullets, Lanjesi Nkhoma ndipo aka ndi koyamba kugoletsa zigoli zambiri kotere.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores