"IFE NGATI DEDZA TATHERA PABWINO" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya Dedza Dynamos, Gilbert Chirwa, wati timu yake yathera pabwino mu ligi ya TNM angakhale kuti anthu amawadelera kuti sangachite bwino.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-1 ndi Ekwendeni Hammers pa bwalo la Rumphi ndipo anati Ekwendeni inabwera mwamphamvu kwambiri komabe ndiwokondwa kuti athera pa nambala yabwino.
"Anali masewero ovuta kwambiri anzathuwa anatipanikiza kwambiri mwina poti anali pa ngozi nde tinachinyitsa zigoli ziwiri koma chigawo chachiwiri tinasewera bwino mpaka tinapeza chigoli koma tathera pa nambala 7 ndipo tonse takondwa kwambiri." Anatero Chirwa.
Timu ya Dedza Dynamos yathera pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7) pomwe yatolera mapointsi okwana 38 pa masewero 30 omwe yasewera.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores