"TIGERS NDI TIMU YAIKULU SINGATULUKE" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers, Christopher Nyambose, wati ananeneratu kuti Tigers ndi dzina lalikulu ndikuti singatuluke mu ligi ndipo zatsimikizika mtsiku lamulungu pa bwalo la Dedza.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 0-0 ndi timu ya Kamuzu Barracks ndipo wati anali masewero ovuta kwambiri pomwe KB inabwera mwamphamvu kwambiri.
"Anali masewero ovuta kwambiri poti timasewera ndi timu yabwino komanso inadabwitsa kuti inabwera mwamphamvu kwambiri ngati mwina imamenyera abale awo kuti asatuluke nde komabe timayenera kuzimenyera nkhondo mpaka zatheka." Anatero Nyambose.
Iye anati timu yake inakumana ndi mavuto kamba koti anasintha osewera 7 atabwera kumene ndipo wathokoza SULOM kamba koyendetsa bwino ligiyi. Tigers yamaliza pa nambala 11 ndi mapointsi okwana 36 mu ligiyi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores