"NDINE WOKONDWA KUTI NDADUTSA ZOMWE NDINAPATSIDWA" - MTETEMERA
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, MacDonald Mtetemera, wati kuthera pa nambala yachinayi mu ligi ya TNM ndi chinthu chopambana kwambiri poti wadutsa zomwe amayenera kukwanilitsa.
Iye amayankhula atatha masewero awo omaliza amu ligi omwe apambana 2-1 ndi timu ya Extreme FC ndipo wati ligi ya chaka chino inali yabwino kwambiri kumbali yawo koma wapempha FAM kuyanjana ndi SULOM.
"Inali ligi yabwino kwambiri mutha kuona mpikisano unali wanphamvu kwambiri koma tipemphe a FAM mwina akamapanga masewero amu zikho zina aziwapatsiratu a SULOM kuti asamatipanikize atatero zitha kuyenda bwino." Anatero Mtetemera.
Chitipa yathera pa nambala yachinayi mu ligi ya TNM pomwe yapeza mapointsi 48 pa masewero 30 omwe yasewera mu ligiyi chaka chino.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores