"MGWIRIZANO NDI WOFUNIKA KUTI TIMU IZIPAMBANA" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Abel Mkandawire, wati mgwirizano wawo womwe uliko pakati pa aphunzitsi komanso osewera ndi omwe wathandiza kuti timuyi ichite bwino mu chaka chawo choyamba cha ligiyi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa Karonga United 3-0 lamulungu ndipo wati iye amayanjana bwino ndi aphunzitsi anzake komanso osewera onse omwe ndi akatswiri kutimuyi.
"Tithokoze Mulungu kamba koti tamaliza motere tithokozenso aphunzitsi anzanga Joseph Kamwendo, Semu ndi ena komanso osewera eni ake poti tagwira ntchito yabwino ndipo mgwirizano umenewu watithandiza kutsala mu ligiyi." Anatero Mkandawire.
Iye wati mpikisano wa chaka chino unali wovuta kwambiri komabe iwo akwanitsa kuchita bwino poti akamati Stars ndi kutanthauza kuti anali ndi akatswiri apamwamba okhaokha.
Bangwe yamaliza pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) ndi mapointsi 42 pa masewero 30 yomwe yasewera mu ligiyi.
Wolemba: Hastings Wadza K
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores