"TADZIMENYERA NKHONDO TOKHA" - CHIDATI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Civo United, Wilson Chidati, wati ndi wosangalala poti timu yake yatsalira mu ligi ndipo wati anyamata anazimenyera nkhondo okha.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonjetsa Mighty Mukuru Wanderers 1-0 pa bwalo la Civo lamulungu ndipo anati zotsatirazi zawathandiza kwakukulu chifukwa tsoka lililonse ndekuti imatuluka ndi iyoyo.
"Zotsatira zabwino kwambiri zomwe zatithandiza kuti tisatuluke mu ligi, anali masewero ovuta kwambiri potengera kuti anzathuwa amafuna amalize pamtunda pang'ono koma timayenera kuti tizimenyere nkhondo. Tatsala ndi masewero mu Castel Cup ndi pomwe tione chitsogolo chathu." Anatero Chidati.
Kupambana kwa Civo kwapangitsa timuyi kulowa mu ndandanda wa matimu asanu ndi atatu oyambilira mu ligiyi pomwe yathera pa nambala 8 ndi mapointsi 38 pa masewero 30.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores