"TSOPANO NDIKUDERA NKHAWA NDIPO NDILI NDI MANTHA" - CHINGOKA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks wati ali ndi mantha tsopano ndi tsogolo la timuyi mu ligi ya TNM pomwe wati masewero awo ndi MAFCO amayenera kupambana.
Iye amayankhula atatha masewero omwe analepherana 1-1 pa bwalo la Mzuzu ndipo wati oyimbira wawakanira zigoli ziwiri zoonekeratu koma kufanana mphamvuku kwapereka mantha kwa iyeyo.
"Pakadali pano ndili ndi mantha kwambiri ndipo ndikudera nkhawa chifukwa timayenera kupambana mmasewero awawa koma tsopano sindikudziwa kuti mmasewero ena akubwerawa anzathu amaliza motani." Anatero Chingoka.
Timu ya Moyale ili ndi mapointsi 32 pa masewero 29 pa nambala 14 ndipo ikuyenera kukumana ndi timu ya Red Lions yomwe inatuluka kale mu masewero awo omaliza amu ligi ya TNM.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores