"LIGI YA CHAKA CHINO INALI YOVUTA" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Pritchard Mwansa, wati ligi ya chaka chino ya TNM inali yovuta kwambiri pomwe wati matimu omwe ali abwino avutika kwambiri.
Iye amayankhula atatha masewero omwe analepherana 1-1 ndi timu ya Moyale Barracks pa bwalo la Mzuzu ndipo wati masewerowa anali ovuta kwambiri komabe kutenga point imodzi koyenda ndi zowathandizabe.
"Anali masewero ovuta kwambiri kutengera kuti tonse tili kumunsi komanso ndi Red Card yomwe tinapeza mwina inatisokonezabe pang'ono koma point ndi yambiri koyenda kungoti mmene tilili sitimayenera kukhala malo omwe tili, timu ndi yabwino koma zotsatira zikuvuta." Anatero Mwansa.
Iye wati ayesetsa kuti akonze mofooka monse kuti akamadzakumana ndi Blue Eagles adzachite bwino. Timuyi ili pa nambala 12 ndi mapointsi 34 pa masewero 29 omwe yasewera mu ligiyi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores