"TIKUYENERA TIZIGWIRIRE NTCHITO TOKHA" - CHIDATI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Civo United, Wilson Chidati, wati timu yake ili ndi ntchito yoti izigwirire yokha kuti itsale mu ligi pomwe ikukasewera ndi Mighty Mukuru Wanderers mmasewero awo omaliza amu ligi.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe analepherana 2-2 ndi timu ya Bangwe All Stars pa bwalo la Mpira ndipo wati point imeneyi iwathandiza kwambiri koma ali ndi ntchito ndi Wanderers.
"Ndi nthawi yoti tizimenyere nkhondo tokha nde apa tikupita pakhomo pa bwalo lathu pomwe tikudziwa pomwe limalekezera nde tikakagwiritsa ntchito mwayi wosewera pakhomo ndikukhulupilira zikatithandiza." Anatero Chidati.
Timu ya Civo ili pa nambala 11 mu ligi ya TNM pomwe yatolera mapointsi okwana 34 pa masewero 29 omwe yasewera.
Wolemba Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores