"CHIGOLI CHAWO CHACHIWIRI SINDINAGWIRIZANE NAZO" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Abel Mkandawire, wati kufanana mphamvu ndi timu ya Civo United ndi chamuna chomwe poti Civo inabwera mwamphamvu kuti isatuluke mu ligi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe matimuwa alepherana 2-2 pa bwalo la Mpira koma wati chigoli chachiwiri cha Civo United, oyimbira akanatha kuchita bwino.
"Palibe chomwe chinavuta kwambiri ndi mmene masewero amayenera kukhalira poti anzathuwa akufuna asatuluke muligi komabe chigoli chachiwiri chija mwina oyimbira akanatha kuyimitsa mpira komabe poti chiganizo chake ndi chomaliza." Anatero Mkandawire.
Pa chigolichi, wosewera wa Bangwe All Stars anagwa ndipo madotolo amakamuona ndipo osewera ena anapita kukamwa madzi ndipo oyimbira anayambitsa masewerowa ena ali panja ndipo Binwell Katinji anagoletsa chigoli chachiwiri.
Timu ya Bangwe tsopano ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) pomwe ili ndi mapointsi 39 pa masewero 29 omwe asewera.
Wolemba
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores