CHIMPWIRIKITI MU AIRTEL TOP 8
Timu imodzi ikuyembekezeka kufika mu ndime yotsiriza ya chikho cha Airtel Top 8 pomwe ena ali mu ndime yamatimu asanu ndi atatu a chikhochi pomwe matimu a Blue Eagles ndi FCB Nyasa Big Bullets akukumana lamulungu pa bwalo la Bingu.
Bungwe la Football Association of Malawi lapitilirabe ndi ganizo lopitiliza masewero pakati pa Blue Eagles ndi Bullets angakhale kuti anayimitsa a Mighty Mukuru Wanderers ndi Silver Strikers amu ndime ya matimu asanu ndi atatu kamba ka milandu yomwe ikukambidwa.
Milanduyo yakambidwa lachisanu pakati pa bungweli ndi Mighty Mukuru Wanderers ndipo chiganizo chituluka mmasiku akudzawa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores