"NDIKUKHULUPILIRA KUTI MOYALE SITULUKA" - CHINGOKA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Victor Chingoka, wati timu yake sikutuluka mu ligi ndipo ayesetsa kuti amalize bwino mmasewero awo omwe atsala nawo kuti ligi ya chaka cha mawa adzayambire pamenepo.
Iye amayankhula izi patsogolo pa masewero awo ndi MAFCO loweruka ndipo wati akudziwa kuti akhala masewero ovuta kutengera kuti matimu onse ali pa ngozi yotuluka mu ligi ngati sachita bwino.
"Kukonzekera kwathu takonzekera monga mwa nthawi zonse komabe tikudziwa kuti masewero akhala ovuta chifukwa anzathuwa abweranso kuti asunge malo amu ligi komabe ifeyo tikufunitsitsa kuti timalize bwino kuti chaka cha mawa tidzayambire pamenepo. Moyale sikutuluka mu ligi." Anatero Chingoka.
Timu ya Moyale ili pa nambala yachikhumi ndi chinayi (14) pomwe ili ndi mapointsi 31 pa masewero 28 omwe yasewera mu ligiyi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores