"TITHOKOZE ANYAMATA POTI ANALIMBIKIRA" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya Dedza Dynamos, Gilbert Chirwa, wayamikira anyamata ake kamba kochilimika mpaka kugonjetsa timu ya FCB Nyasa Big Bullets ndipo wati anakambirana zoti ayidzidzimutse Bullets.
Iye amayankhula izi atagonjetsa FCB Nyasa Big Bullets 1-0 pa bwalo la Dedza ndi chigoli cha Clement Nyondo mu mphindi yoyamba ndipo wati anyamata ake agwira ntchito yotamandika.
"Analidi masewero ovuta kwambiri koma anyamata anachilimika, anatsatira chimene timawauza kuti Bullets imapita kwambiri kutsogolo nde titseke mipata yonse nde anyamata apanga zimene tinawauza komanso tinakambirana kuti tidzidzimutse Bullets." Anatero Chirwa.
Timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chitatu (8) pa masewero 29 omwe yasewera ndi mapointsi 38 ndipo yatsala ndi masewero amodzi kuti amalize ligi ya chaka chino.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores