CHITIPA UNITED YAPAMBANA MPHOTO KU MPOTO AWARDS
Timu ya Chitipa United yasankhidwa kukhala timu yapamwamba mu chaka cha 2023 itagonjetsa matimu ena anayi mmavoti kamba koti inapeza ochuluka kwambiri kuposa enawo.
Chitipa inagonjetsa timu ya Karonga United ndi Ekwendeni Hammers, onse amu Supa ligi komanso ena awiri amu Basketball a Nkhande komanso Pistons akumpoto komweko.
Kumbali ya wosewera wapamwamba kuposa onse ku matimu akumpotowa, Priscilla Soko wa Chimwavi Smashers ndi yemwe wapamwamba atagonjetsa Macdonald Harawa ndi Gastin Simkonda a Moyale Barracks komanso Jimmy Msiska wa Ekwendeni Hammers.
Aka kanali koyamba kuti a mpoto awards apereke mphoto kumbali ya zamasewero ndipo mphotozi zimapita kwa anthu okha okha ndi matimu akumpoto kwa dziko lino.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores