GABA WATSALA KU LIBERIA
Timu ya Flames sikhala ndi katswiri wawo wa kutsogolo, Gabadinho Mhango, mmasewero omwe akumane ndi timu ya Liberia mu masewero opitira ku World Cup kamba koti ndege yopita ku Ethiopia yamuthawa.
Katswiriyu amayenera kunyamuka mdziko la South Africa lamulungu kuti akakumane ndi timu yonse ku Ethiopia pa ulendo wawo opita ku Liberia koma wasemphana nayo ndegeyi.
Timuyi sikhalanso ndi katswiri wa Pakati ku FCB Nyasa Big Bullets, Frank Willard, yemwe wavulala mmasewero omwe timu yake inalepherana 0-0 ndi Blue Eagles.
Osewera atatu, Christopher Kumwembe, Olson Kanjira komanso Mhango ndi omwe anatengedwa kuti akasewere kutsogolo kwa timuyi ndipo Chifundo Mphasi ndi Lanjesi Nkhoma ndi ena omwe atha kulowa mmalo mwa katswiriyu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores