"ZOTI NDASEWERAPO KAPENA KUPHUNZITSA WANDERERS SI MWAYI" - KAMWENDO
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Joseph Kamwendo, wati sizikutanthauza kuti timu yake itha kugonjetsa Mighty Mukuru Wanderers mophweka poti iyeyo wakhalitsako koma wati kuwina kukhala kofunikira.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero omwe matimuwa akukumana lamulungu pa bwalo la Kamuzu ndipo wati akuyembekezera kuti masewero akhala ovuta kwambiri.
"Zoti ndasewerako kapena kuphunzitsa Wanderers ndizoona koma panopa ndine mphunzitsi zimenezo sizikutipatsa mwayi uliwonse ndipo masewero akakhala ovuta poti tikukumana ndi timu yabwino koma tikayesetsa kuti tikapambane kuti tikhalebe mu top 8." Anatero Kamwendo.
Kamwendo sali nawo pa gulu la osewera akale a Flames omwe apita ku Zambia kukasewera ndi osewera akale amdzikomo loweruka. Bangwe ili pa nambala yachisanu ndi chiwiri pa masewero 26 omwe yasewera ndi mapointsi 35.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores