FAM YATULUTSA MAYINA APA MPHOTO ZA FDH
Bungwe loyendetsa mpira mdziko muno la Football Association of Malawi latulutsa mayina omwe alimbirane pa mphoto zisiyanasiyana za mu chikho cha FDH Bank chomwe chinatha mmasabata awiri apitawa.
Bungweli latulutsa mayinawa lachinayi ndipo laika omwe apikisane pa yemwe wasewera bwino mpikisano onse, goloboyi wabwino, womwetsa zigoli zambiri komanso osewera waluso watsopano.
Wosewera pakati ku FCB Nyasa Big Bullets, Patrick Mwaungulu, Paul Ndhlovu wa MAFCO ndi Clement Nyondo wa Dedza Dynamos alimbirana pa mphoto ya osewera wapamwamba mu chikhochi pomwe goloboyi wa Santhe ADMARC, Zahaya Malithano, William Thole wa Wanderers ndi Rabson Chiyenda wa Bullets alimbirana pa goloboyi wapamwamba.
Ephraim Kondowe wa Bullets, goloboyi wa Santhe, Zahaya Malithano ndi goloboyi wa Extreme, Mclean Mwale ndi omwe apikisane pa mphoto ya luso lapamwamba latsopano ndipo Hassan Kajoke ndi yemwe anamwetsa zigoli zambiri.
Timu ya Bullets inatenga ukatswiri wa chikho
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores