NKHAKANANGA NDI ENA ANAYI ALANDIRA ZILANGO
Bungwe la FAM ndi limene latulutsa zilangozi pomwe Nkhakananga amupeza olakwa kamba kosaimitsa mpira ataimba wezulo ndi kulora chigoli cha Silver Strikers pa 23 September 2023 ndipo saimbira kwa miyezi inayi.
Ndipo oyimbira, Dave Chambo, wapatsidwa chilango chosaimbira kwa miyezi inayi kamba kosaimbira bwino pomwe Silver ilepherana 0-0 ndi Chitipa United pa 1 August 2023.
Oyimbira wina, Peter Jossam, yemwe anakana penate pomwe Blue Eagles inagonja 2-1 ndi Silver Strikers pa 6 August yoonekeratu sayimbira kwa miyezi itatu.
Deus Nyirongo sapezeka miyezi inayi atasokoneza masewero a Chitipa United ndi Karonga United pa 22 April ndipo yemwe amayang'anira masewerowa, Zuza Nyondo, amupatsa chilango cha miyezi inayi kamba kolemba lipoti yabodza komanso poonetsa kusadziwa kwa malamulo a mpira atayitanidwa ndi FAM.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores