MPIRA WAMIYENDO WA AMAYI WALANDIRA THANDIZO LA UZIMU
Mbiri yalembedwa pomwe mpira wamiyendo koma ali amayi walandira thandizo lokwana K50 million kuchokera ku Goshen City yomwe ithandizire mu ligi ya amayiwa komanso timu ya dziko lino pomwe ikupita ku mpikisano wa COSAFA mwezi wa mawa.
Mgwirizano wa ndalamayi wasainidwa ku malo ogonerako a Golden Peacock ku Lilongwe pomwe wamkulu wa Goshen, Prophet Shepherd Bushiri, Mkulu wa bungwe la FAM, Walter Nyamilandu Manda komanso mkulu wa mpira wamiyendo wa amayi, Adellaide Migogo, anasainirana mgwirizanowu.
Ndalama zokwana K29 million zikupita ku mayendedwe ndi zina zambiri za Scorchers pomwe ikupita ku South Africa ndipo K21 million ikupita ku ma ligi a FAM Women's Football league omwe tsopano azitchedwa Goshen Women's Football league.
Bushiri waperekanso K10 million yoonjezera yopita kwa atsikana a Scorchers ku nkhani ya ndalama zimene amalandira.
Photo: FAM Media
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores