MALAWI IKULINGAKIRA ZOCHITITSA AFCON MU 2029
Mtsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi, Dr Walter Nyamilandu Manda, wati akulingalira zolumikizana ndi mayiko a Botswana ndi Zambia kuti akapereke pempho lochititsa mpikisano wa African Cup of Nations mu 2029 limodzi.
Nyamilandu wayankhula izi dzana pomwe amayamikira mayiko a Kenya, Tanzania ndi Uganda kamba kopambana pempho loti achititse mpikisanowu mu 2027. Iye wati dziko la Malawi likhonza kuchititsa nawo mpikisanowu poti lili ndi kuthekera.
"Zawonetsera poyela kuti COSAFA ikhonzanso kupambana itati yakonzekera komanso kugwirizana bwino. Ndikutha kuwona Malawi ikupereka moto itati yajoina bidi ya Botswana ndi Zambia mu 2029. Palibe chifukwa chotsalira mbuyo. Dziko lathu liri ndi upangili okwanila." Anatero Nyamilandu polemba pa Facebook.
Dziko la Ivory Coast ndi limene lichititse mpikisanowu mu chaka cha mawa ndipo Morocco idzauchititsa mu 2025. Dziko la Malawi silinachititseko mpikisano ngati umenewu.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores