"WANDERERS SITIMAYIOPA" - SANKHANI
Katswiri wotseka kumbuyo wa timu ya Blue Eagles, Sankhani Mkandawire, wati akudziwa kuti masewero omwe timu yake ikukumana ndi Wanderers akhala ovuta koma samayiopa timuyi.
Sankhani amayankhula izi pomwe matimuwa akumane pa bwalo la Nankhaka lachitatu ndipo wati akukhulupilira kuti apambana masewerowa.
"Ndi masewero ofunika kwambiri mukudziwa kuti nyengo zathu mmbuyomu zinali zovuta koma tithokoze Mulungu poti watisinthira nyengo ndipo tili ndi chikhulupiliro kuti tipeza chipambano kuti pa log table paja zizioneka mmene zikuyenerera kukhalira." Anatero Sankhani.
Iye anati timu ya Mighty Mukuru Wanderers wakumana nayo kwambiri ndipo ndi masewero aakulu koma samayiopa ndipo amangoyipatsa ulemu. Eagles ili pa nambala yachisanu ndi chitatu ndi mapointsi 30.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores