BABATUNDE WAPEREKA NSAPATO ZOMENYERA MPIRA KWA MWANA OTCHEDWA BABATUNDE
Katswiri wakale wa FCB Nyasa Big Bullets yemwe pano amasewera mu timu ya Venda Football Club ku South Africa, Babatunde Adepoju, wakwanilitsa lonjezo lake pomwe wapereka nsapato zosewera mpira kwa osewera yemwe amatchulidwanso ndi dzina lakeli.
Mwanayu yemwe amasewera mu timu ya bungwe losula maluso a ana la Mpira Mmudzi Mwathu ya osewera osadutsa zaka 16, walandira nsapatozi lachiwiri pomwe Babatunde anasangalatsidwa ndi zomwe tsamba la bungweli linalemba za osewerayu.
Katswiri wakale wa Scorchers, Linda Kasenda, ndi yemwe anapereka nsapatozi mmalo mwa katswiriyu yemwe ali mdziko la South Africa.
Mwanayu apatsidwa dzinali kamba ka luso lake la kaseweredwe ndi mamwetsedwe a ntibu wa zigoli zimene zimafanana ndi katswiri waku Nigeriayu.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores