NKHAKANANGA AKUCHITA NAWO MAPHUNZIRO A OYIMBIRA
Oyimbira odziwika bwino mdziko muno, Godfrey Nkhakananga, pamodzi ndi oyimbira ena mdziko muno akuchita nawo maphunziro ozindikiritsa malamulo a ntchito yawo ku Mpira house ku Chiwembe ku Blantyre.
Maphunzirowa omwe ndi amasiku asanu, akutsogozedwa ndi nthumwi ya FIFA, Carlos Henriques yemwe wapempha oyimbirawa kuti azitha kuulula matimu omwe amasapotera kuopa kugwira ntchito yokondera matimu awowa.
Ndipo mkulu wa komiti ya oyimbira ku FAM, Rashid Mtelera, walangiza oyimbirawa kuti azigwira ntchito yotamandika ponena kuti anthu ambiri akuwadandaula pa kagwiridwe ntchito yawo.
Kupatula Nkhakananga, nkhope za oyimbira enanso odziwika bwino omwe ali nawo maphunzirowa ndi monga Gift Chiko, Mwayi Msungama, Mayamiko Kanjere, Bernadettar Kwimbira, Happiness Mbandambanda ndi ena.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores