UNDUNA NDI FAM ADZUDZULA MCHITIDWE WOONONGA MIPANDO PA BWALO LA BINGU
Mipando yokwana 80 ndi imene inaonongedwa kutsatira zisokonezo zimene zinachitika pa bwalo la Bingu pomwe matimu a Silver Strikers ndi Mighty Mukuru Wanderers anakumana mu chikho cha Airtel Top 8 sabata yatha, akuluakulu a bwaloli atsimikiza.
Zipolowe zinayamba Godfrey Nkhakananga atapereka chigoli kutimu ya Silver Strikers angakhale kuti anaimba kuti mpira uime poti osewera wa Wanderers anagwira mpira.
Koma akuluakulu a unduna wa zamasewero komanso bungwe la Football Association of Malawi ladzudzula mchitidwe oononga mipandoyi pomwe ati bwaloli ndi lokha limene linatsala mdziko muno lovomerezeka ndi CAF ndiye liyenera kusamalidwa.
Ochemerera atimu ya Mighty Mukuru Wanderers ndi omwe anaononga katunduyu ndipo timuyi ikhonza kulipira ndalama ya chindapusa pa mlanduwu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores