"TIKUFUNA TIKAFIKE MU NDIME YOTSIRIZA KU COSAFA" - FAZILI
Mphunzitsi watimu ya Scorchers, Lovemore Fazili, wati timu yake yaika mulingo ofuna kukathera mu ndime yotsiriza ya chikho cha COSAFA Women's Championship omwe achitike mu mwezi wa mawa mdziko la South Africa.
Iye amayankhula izi patsogolo pa aubale omwe timuyi isewere lolemba ndi dziko la Seychelles ndipo iye wathokoza FAM kamba kowapezera masewero aubale koyamba asanapite ku mpikisano. Iye wati timu yake ikuyang'ana zothera mu ndime yotsiriza ku COSAFA.
"Mwina Seychelles papepala ikuoneka ngati yofooka potengera kuti Scorchers ili patsogolo pawo koma masewero aliwonse anathandizira kusintha chinachake so zitithandiza kuona mmene osewera agwirirana ndi khalidwe lawo mu bwalo. Tili ndi timu yabwino ndipo target yathu ndi yokafika ndime yotsiriza." Anatero Fazili.
Matimuwa asewera masewerowa pa bwalo la Mpira lero ndipo adzakumananso lachinayi mmasewero ena. Mpikisano wa COSAFA uyamba pa 04 October mpaka pa 15 October 2023.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores