"KUTENGA LIGI KUTIVUTA KOMA KUKHALABE MULIGIMU" - CHINGOKA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Victor Chingoka, wati wauza osewera ake kuti asagone chifukwa choti atuluka ku malo a matimu otuluka mu ligi koma akuyenera kuchilimbika kwambiri poti sali otetezekabe.
Iye amayankhula izi kutsatira kupambana 2-0 ndi timu ya Extreme FC pa bwalo la Nankhaka ndipo wati ndi okondwa kamba ka chipambanochi. Iye wapempha osewera ake kuti achilimike kuti akhalebe mu ligiyi.
"Mukuona mmene ligi yavutiramu sitili pabwinobe nde tawauza osewera kuti apeze zipambano mwina mmasewero atatu kapena anayi zimenezi zitha kutikhalira bwino." Anatero Chingoka.
Iye wati vuto lalikulu lili komwetsa zigoli ndipo ayesetsa kukonza zinthuzi kuti izipeza zigoli. Moyale yafika pa nambala 11 pomwe ili ndi mapointsi 26 mmasewero 22 omwe asewera.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores