"TIKUYENERA TIPAMBANE MMASEWERO ONSE ATSALAWA" - M'GANGIRA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Silver Strikers, Peter M'gangira, wati za kugonja kwawo ndi Dedza Dynamos zapita ndipo akuyang'ana za kutsogolo pomwe akufuna kupambana mmasewero awo onse omwe atsala mu ligi.
Iye amayankhula atatha masewerowa omwe anagonja 1-0 pa bwalo la Champions ndipotu wati kuphonya kwambiri ndi kumene kwawaluzitsa mmasewerowa.
"Tinali ndi mipata yambiri yomwe takanika kugoletsa makamaka mchigawo chachiwiri koma basi tagonja 1-0 tikuyenera kuyang'ana chitsogolo kuti mwina masewero atsalawa titolere mapointsi atatu iliyonse." Anatero M'gangira.
Timu ya Silver Strikers inaona katswiri wawo, Chimwemwe Idana, akupezeka makamaka mchigawo chachiwiri komabe sizinaletse Dedza kupambana. Silver ikadali pa nambala yachinayi pomwe ili ndi mapointsi 36 pa masewero 21.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores