"SAIZI ALI NDI LUSO LOSAKAKAMIZA" - MKANDAWIRE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Abel Mkandawire, wayamikira katswiri wawo, Robert Saizi, kuti ali ndi luso lamtengo wapatali pomwe wati ndi osewera ofunikira kwambiri kutimuyi.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe anagonjetsa Red Lions 2-0 pa bwalo la Balaka ndipo Saizi anatenga mphoto yoti wasewera bwino pomwe anagoletsa chigoli chachiwiri mmasewerowa. Iye wati kupambana kwa timuyi ndi kofunikira kwambiri.
"Anali masewero ovuta kwambiri chifukwa Red Lions inabweranso kuti ipeze chipambano koma tinawauza osewera kuti akhazikitse mtima pansi pomwe tipeze mwayipo tigoletse. Saizi ndi luso losowa kwambiri, zosachita kukakamiza ndipo tinamusowa kwambiri ndi Chitipa." Anatero Mkandawire.
Chipambano cha Bangwe All Stars chaifikitsa pa nambala 6 pomwe yatolera mapointsi 31 pa masewero 22 omwe yasewera.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores