"KUMWEMBE SANAMALIZE KUTIGWIRITSA NTCHITO" - MPINGANJIRA
Mkulu watimu ya timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Roosevelt Mpinganjira, wati timu yawo sinathane ndi katswiri wawo Christopher Kumwembe pomwe amukaniza kuti apite kutimuyi ya Green Buffaloes yaku Zambia yomwe inamufuna.
Zinamveka kuti timu ya Buffaloes imafunitsitsa Kumwembe ndipo inalembera Wanderers ndipo timuyi inaika Kumwembe pa mtengo wa $80 million yomwe Buffaloes imafuna mtengowu utsitsidwe koma Manoma amakana.
Mpinganjira wati analandira kalata ndithu yochokera kutimuyi komatu iwo sali okonzeka kugulitsa Kumwembe.
"Kalata tinalandiradi koma tsopano sitinali okonzeka kumugulitsa Kumwembe chifukwa tinamugula kuti atigwirire ntchito ndipo ntchito akadzagwira tidzamulora kuti achoke." Mpinganjira anafotokoza.
Buffaloes inaona Kumwembe kutimu ya Flames pomwe anali ku COSAFA ndipo katswiriyu ali ndi zigoli zokwana zisanu ndi ziwiri mu ligi ya chaka chino.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores